Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 2:15 - Buku Lopatulika

15 nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 2:15
17 Mawu Ofanana  

Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake.


Adzazulidwa kuhema kwake kumene anakhulupirira; nadzatengedwa kunka naye kwa mfumu ya zoopsa.


Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa; pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.


Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.


Mtima wanga uwawa m'kati mwanga; ndipo zoopsa za imfa zandigwera.


Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.


Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?


Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!


kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?


Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.


Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa