Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Amanenanso kuti, “Ndidzakhulupirira Mulungu.” Penanso amanena kuti, “Ine ndili pano, pamodzi ndi ana amene Mulungu adandipatsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndiponso, “Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.” Ndiponso Iye akuti, “Ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Mulungu wandipatsa.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 2:13
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.


Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.


Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.


Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.


Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.


Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa