Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 13:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti pano tilibe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 13:14
18 Mawu Ofanana  

Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.


Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;


Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.


Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.


Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali.


Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.


Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa