Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 13:12 - Buku Lopatulika

12 Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 13:12
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.


Pamenepo khamu lonse linamtulutsa kunja kwa chigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.


nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, nanka naye pamutu paphiri pamene panamangidwa mzinda wao, kuti akamponye Iye pansi.


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;


Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.


Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi malayawo, ndi chikute chagolide, ndi ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ng'ombe zake, ndi abulu ake, ndi nkhosa zake, ndi hema wake ndi zake zonse; nakwera nazo ku chigwa cha Akori.


Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa