Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 10:2 - Buku Lopatulika

2 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 10:2
8 Mawu Ofanana  

Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.


Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.


ndipo machimo ao ndi kusaweruzika kwao sindidzakumbukiranso.


Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa