Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 1:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe? Ndiponso, Ine ndidzakhala kwa Iye Atate, ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe? Ndiponso, Ine ndidzakhala kwa Iye Atate, ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 1:5
8 Mawu Ofanana  

Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;


iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wake; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wake pa Israele, kosalekeza.


Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.


Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


Koteronso Khristu sanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa