Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 4:10 - Buku Lopatulika

10 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndakondwa kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano, patapita nthaŵi yaitali, mwayambanso kuwonetsa kuti mumandikumbukira. Kukumbukira munkandikumbukiradi, koma munkangosoŵa mpata woti muwonetsere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 4:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.


ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.


m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,


Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;


pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa