Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 2:10 - Buku Lopatulika

10 kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 2:10
17 Mawu Ofanana  

ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu aamuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadire Baala.


kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.


Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate,


Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?


Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.


Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.


akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,


Ndipo sanathe mmodzi mu Mwamba, kapena padziko, kapena pansi padziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa