Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 1:18 - Buku Lopatulika

18 Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Zili nkanthu ngati! Kaya amalalika mwachiphamaso, kaya moona, malinga nkuti Khristu akulalikidwa, pamenepo ine ndikukondwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi. Ndithu, ndidzapitirira kukondwera,

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 1:18
13 Mawu Ofanana  

Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.


Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.


Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.


Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;


Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai.


Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?


Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.


Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira.


Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa