Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 2:7 - Buku Lopatulika

7 kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adachita zimenezi kuti mwa chifundo chake chimene adatichitira mwa Khristu Yesu, aonetse kwa nthaŵi zonse zam'tsogolo kuti ngwokomadi mtima kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 2:7
13 Mawu Ofanana  

Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.


Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?


Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,


koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,


kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.


chimene sanachizindikiritse ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu,


kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka,


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa