Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 2:5 - Buku Lopatulika

5 tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 2:5
20 Mawu Ofanana  

chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.


Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.


Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.


Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe.


Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;


Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;


Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.


Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Khristu anawafera osapembedza.


Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.


Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.


Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,


Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;


Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.


Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;


Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,


zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi oyera mtima onse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa