Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 2:16 - Buku Lopatulika

16 ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 2:16
14 Mawu Ofanana  

Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.


podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.


Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.


Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.


atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;


kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,


Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu;


adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;


Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa