Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 2:12 - Buku Lopatulika

12 kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 2:12
51 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;


Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira.


Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko.


Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.


Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.


Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.


Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yampesa.


Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m'dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.


Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.


Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;


Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.


Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.


Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda.


Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.


Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu.


Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.


Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.


Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;


Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;


Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo,


kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;


chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;


Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;


Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa