Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 2:11 - Buku Lopatulika

11 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu).

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 2:11
29 Mawu Ofanana  

Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita.


Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.


Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.


Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,


Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe?


Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?


Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitili ochimwa a kwa amitundu;


Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.


zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;


pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo mu Ejipito; musamalire kuchita malemba awa.


Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo,


amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;


Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;


pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa