Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 1:1 - Buku Lopatulika

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndikulembera anthu a Mulungu amene ali ku Efeso, amenenso ali okhulupirika mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu. Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 1:1
27 Mawu Ofanana  

Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.


Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.


Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu mu Yerusalemu;


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.


ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;


Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali mu Akaya monse:


Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),


Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.


Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,


Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.


ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;


Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;


kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a mu Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.


Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa