Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Yohane 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa mai wosankhidwa ndi Mulungu, ndi kwa ana ake amene ndimaŵakonda kwenikweni. Ndipo sindine ndekha amene ndimakukondani, komanso onse odziŵa choona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndine mkulu wampingo, kulembera: Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi.

Onani mutuwo Koperani




2 Yohane 1:1
25 Mawu Ofanana  

kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;


ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.


ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.


Moni kwa Rufu, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wake ndi wanga.


Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?


Koma sitidawafumukire mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu.


Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?


Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?


chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,


amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.


Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:


Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.


Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.


Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.


Akupereka moni ana a mbale wanu wosankhika.


Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake.


Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa