Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 4:4 - Buku Lopatulika

4 ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 4:4
13 Mawu Ofanana  

Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.


Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;


kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;


koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;


Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;


Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene.


osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.


Chisomo chikhale ndi inu nonse, Amen.


Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa