Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 2:8 - Buku Lopatulika

8 Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali mmodzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 2:8
18 Mawu Ofanana  

Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;


Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,


tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.


Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;


kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.


monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.


umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.


Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;


Lingirira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m'zonse.


ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa