Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 1:1 - Buku Lopatulika

1 Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa mu Khristu Yesu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Khristu Yesu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa kufuna kwa Mulungu. Adandituma kuti ndilalike chilonjezo cha moyo umene uli mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu. Anandituma kuti ndilalike za lonjezo la moyo umene uli mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 1:1
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa.


Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.


Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.


Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.


Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali mu Akaya monse:


Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.


Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,


nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.


koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,


Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.


ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;


kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.


Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.


Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa