Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 8:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:4
8 Mawu Ofanana  

Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.


Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'mizinda yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu mu Yerusalemu.


Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.


Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.


Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa