Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 8:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:4
8 Mawu Ofanana  

Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri, kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo, pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.


Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu.


Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.


Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.


Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.”


Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”


Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa