Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 3:25 - Buku Lopatulika

25 Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Inu amfumu, monga Abinere, mwana wa Nere, simumdziŵa? Amene ujatu adaabwera kudzangokumyatani m'maso. Adaafuna kudzangokutambwani, kuti adziŵe zonse zimene mukuchita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:25
16 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.


Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.


Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.


Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?


Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi.


Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.


Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.


wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.


Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.


Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?


Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.


Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa