2 Samueli 23:8 - Buku Lopatulika8 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Naŵa maina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti, wa ku Takemoni, mkulu wa atsogoleri ankhondo atatu. Iye adaamenyana nkhondo ndi anthu 800, naŵapha onsewo ndi mkondo wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi. Onani mutuwo |
Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.