Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 21:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 adapita kukatenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wa Saulo. Adaŵachotsa m'manja mwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, amene adaaba mafupawo ku bwalo la ku Beteseani, kumene Afilisti adaaŵanyonga, tsiku limene Afilistiwo adapha Saulo ku Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa).

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 21:12
15 Mawu Ofanana  

Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.


Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.


Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.


Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Saulo anachita.


nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa.


Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa paphiri la Gilibowa.


anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.


Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa paphiri la Gilibowa.


Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.


Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.


Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa.


Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo.


Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa