2 Samueli 18:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Zitatero, Ahimaazi uja, mwana wa Zadoki, adauzanso Yowabu kuti, “Zitanizitani, mundilole kuti inenso ndimthamangire Mkusi uja.” Yowabu adamufunsa kuti, “Mwana wanga, chifukwa chiyani ukuti uthamange, pamene sudzalandirapo mphotho chifukwa cha uthenga umenewo?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Ahimaazi mwana wa Zadoki ananenanso kwa Yowabu kuti, “Zivute zitani, chonde mundilole kuti ndipite pambuyo pa Mkusiyo.” Koma Yowabu anayankha kuti, “Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukufuna kupita? Ulibe nkhani yoti ukalandire nayo mphotho.” Onani mutuwo |