Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Pambuyo pake Yowabu adauza Mkusi kuti, “Pita, ukauze mfumu zimene waziwonazi.” Mkusiyo adaŵeramira Yowabu mwaulemu, nayamba kuthamanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kenaka Yowabu anawuza Mkusi kuti, “Pita ukawuze mfumu zimene waona.” Mkusiyo anawerama pamaso pa Yowabu ndipo anathamanga kupita.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:21
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa.


Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?


Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.


Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa