Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:36 - Buku Lopatulika

36 Onani, ali nao komweko ana aamuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Onani, ali nao komweko ana amuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Ahimaazi, mwana wa Zadoki ndiponso Yonatani, mwana wa Abiyatara, nawonso ali komweko. Ndipo podzera mwa iwowo udzandiwuza zonse zimene udzamve.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Ana awo awiri, Ahimaazi wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiatara ali nawo pamodzi, uzikawatuma kwa ine ndi china chilichonse chimene ukamve.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:36
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumzinda mumtendere pamodzi ndi ana ako aamuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.


Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti.


Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mzinda.


Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa