Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:5 - Buku Lopatulika

5 Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi aakulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi akulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Davide adamva zimenezo, adatuma anthu kuti akaŵachingamire, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye adzabwere kuno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:5
6 Mawu Ofanana  

Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.


Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.


Pamenepo anamuka ena namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anachita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.


Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa