2 Samueli 10:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.” Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi aakulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi akulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono Davide adamva zimenezo, adatuma anthu kuti akaŵachingamire, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye adzabwere kuno.” Onani mutuwo |
Pa nthawi ya Ahabu, Hiyeli wa ku Beteli anamanganso mzinda wa Yeriko. Pa nthawi yomanga maziko ake, mwana wake woyamba wa mwamuna, Abiramu anamwalira, ndipo pa nthawi yomanga zipata zake, mwana wa mngʼono wa mwamuna Segubu, anamwaliranso. Izi zinachitika monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.