Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:10 - Buku Lopatulika

10 Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:10
6 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.


Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu.


Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.


Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.


Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.


Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa