Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Davide adamufunsanso kuti, “Zinthu zidayenda bwanji? Tandiwuza.” Iye adati, “Anthu athaŵa kunkhondoko, ndipo ambirinso aphedwa. Saulo ndi mwana wake Yonatani, nawonso aphedwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?” Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:4
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele.


Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa?


muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Saulo wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilagi, ndiyo mphotho yake ndinampatsa chifukwa cha uthenga wake.


Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa