Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:10 - Buku Lopatulika

10 M'mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 M'mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Choncho ndidasendera pafupi, nkumupha, poti ndidaadziŵa kuti akagwa, sakhala moyo. Tsono ndidamuvula chisoti chaufumu kumutu kwake ndi chigwinjiri kumkono kwake, ndipo ndabwera nazo kuno kwa inu mbuyanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:10
10 Mawu Ofanana  

Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, chifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.


Nachotsa korona pamutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pamutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mzindawo zambirimbiri.


Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.


Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa.


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa