Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 8:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kenaka Solomoni adapita ku Hamatizoba nakaulanda mzindawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 8:3
9 Mawu Ofanana  

Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.


Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?


Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.


Solomoni anamanga mizinda imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israele.


Ndipo anamanga Tadimori m'chipululu, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga mu Hamati.


Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.


kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa