2 Mbiri 4:4 - Buku Lopatulika4 Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi mbuyo zao zinayang'anana. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri: zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuyang'ana kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo miyendo yonse yam'munsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati. Onani mutuwo |