Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono zitatha zaka zisanu ndi ziŵirizo, mai uja adabwerako ku dziko la Afilisti kuja, ndipo adapitanso kwa mfumu ya ku Israele kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.


Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.


Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.


Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.


Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita.


Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino.


Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.


Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa