Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Idafika nthaŵi imene Chauta adafuna kutenga Eliya m'kamvulumvulu kunka kumwamba. Tsiku limenelo Eliya ndi Elisa anali pa ulendo kuchokera ku Giligala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:1
15 Mawu Ofanana  

ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.


Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.


Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.


Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.


Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.


Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kamvulumvulu, nati,


Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,


Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.


Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;


Ndipo anthu anakwera kutuluka mu Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino.


Ndipo anamva mau aakulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa