Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 19:3 - Buku Lopatulika

3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zombalira mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 19:3
13 Mawu Ofanana  

Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m'dzanja lake;


Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.


Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.


Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? Ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? Ati Mulungu wako.


Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa