Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 19:2 - Buku Lopatulika

2 Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 19:2
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.


Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.


Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.


Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.


Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu.


Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,


monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa