Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Ahabu anali nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri mu Samariya. Nalemba makalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mfumu Ahabu anali ndi zidzukulu zazimuna 70 ku Samariya. Tsono Yehu adalemba makalata naŵatumiza ku Samariya kwa olamulira mzindawo, kwa akuluakulu ndiponso kwa anthu amene ankalera zidzukulu za Ahabu kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati,

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:1
14 Mawu Ofanana  

Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.


Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri a siliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mzinda anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho.


Nagona Omuri ndi makolo ake, naikidwa mu Samariya; ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.


Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali mu Samariya, akadamchiritsa khate lake.


Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala mu Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?


Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.


ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;


Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo mizinda makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.


Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.


Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa