Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:8 - Buku Lopatulika

8 Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m'chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m'chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Iwowo adayankha kuti, “Munthuyo adaavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa m'chiwuno.” Apo mfumuyo idati, “Ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwo anayankha kuti, “Munthuyo anavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake.” Mfumu inati, “Munthu ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:8
9 Mawu Ofanana  

Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.


Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?


Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzachita manyazi yense ndi masomphenya ake, ponenera iye; ndipo sadzavala chofunda chaubweya kunyenga nacho;


Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.


Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.


Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa