Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba paphiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pomwepo mfumuyo idatuma mkulu wina wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kukagwira Eliya. Mkuluyo adapita kwa Eliya nampeza atakhala pansi pamwamba pa phiri. Adamuuza kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:9
22 Mawu Ofanana  

Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?


Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.


pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.


Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.


Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.


Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;


ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;


Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, choka, thawira kudziko la Yuda, nudye, nunenere komweko;


Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.


nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?


Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!


Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,


Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.


Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?


kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;


Ndipo pamene anauza Saulo, iye anatumiza mithenga ina; koma iyonso inanenera. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kachitatu, nayonso inanenera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa