2 Mafumu 1:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Amithengawo adayankha kuti, “Kudaabwera munthu kudzakumana nafe, ndipo adatiwuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene idakutumaniyo, mukaiwuze mau a Chauta akuti, “Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni? Nchifukwa chake sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.” ’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Onani mutuwo |