Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Yohane 2:7 - Buku Lopatulika

7 Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Inu okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lakale lomwe lija, limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi. Lamulo lakalelo ndi mau amene mudaŵamva kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:7
22 Mawu Ofanana  

Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.


Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:


Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.


Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe?


ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.


Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;


Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.


Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake:


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu;


Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.


Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.


Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.


Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.


Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa