Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 7:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Choncho Samuele adatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Adapempherera Aisraele kwa Chauta, ndipo Chauta adamuyankha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 7:9
16 Mawu Ofanana  

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.


Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.


Ndipo pakuuka mamawa amuna akumudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi chifanizo chinali pomwepo chitalikhidwa ndi ng'ombe yachiwiri yoperekedwa paguwa la nsembe adalimanga.


Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.


Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.


Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.


Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.


Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.


Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa