Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 6:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono mupange zifanizo za mafundo anu aja ndi za mbeŵa zimene zikuwononga m'dziko mwanu, ndipo mulemekeze Mulungu wa Aisraele. Mwina mwake sadzakuvutaninso, inu ndi milungu yanu ndi dziko lanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 6:5
30 Mawu Ofanana  

Mchitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu, mchitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.


Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.


Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga.


Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.


Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.


Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.


Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m'zisumbu.


Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.


Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.


Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.


Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.


Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.


Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.


Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.


Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.


ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m'bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa