Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 6:18 - Buku Lopatulika

18 ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumilaga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nazonso zifanizo zagolide za mbeŵa adazipereka moŵerengetsa mizinda yonse ya Afilisti imene inali ya akalonga asanu aja. Ina inali mizinda yamalinga, ina inali midzi yapamtetete. Mwala waukulu uja umene adaikapo Bokosi lachipangano lija m'munda wa Yoswa ku Betesemesi, udakalipo mpaka pano ngati mboni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 6:18
4 Mawu Ofanana  

Yonseyi ndiyo mizinda yozinga ndi malinga aatali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.


kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;


Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa