Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsono Davide ndi anthu ake adaŵathira nkhondo namenyana nawo kuyambira mbandakucha mpaka madzulo. Sadapulumukepo Mwamaleke ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu 400 amene adakwera pa ngamira, nathaŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:17
11 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;


za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.


Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.


Nakantha otsala a Aamaleke adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino.


Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.


Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.


Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.


Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.


Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.


Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa