1 Samueli 28:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri. Onani mutuwo |
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.