Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 28:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono Afilisti adasonkhana nadzamanga zithando zao zankhondo ku Sunemu. Saulo nayenso adasonkhanitsa Aisraele, ndipo adamanga zithando ku Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono Afilisti anasonkhana nabwera kudzamanga misasa yawo ku Sunemu. Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kumanga misasa yawo ku Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 28:4
9 Mawu Ofanana  

Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.


Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.


Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;


Tsono anafunafuna m'malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.


Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.


Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu;


Ndipo pamene Saulo anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu.


Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa.


Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa