Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndikumva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitidaŵachite choipa chilichonse, ndipo sadasoŵe kanthu pa nthaŵi yonse pamene adakhala ku Karimele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “ ‘Tsono ndamva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitinawachite china chilichonse choyipa, ndipo sanasowe kanthu pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:7
9 Mawu Ofanana  

Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.


Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.


Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowe kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa